Omenyera ufulu wa anthu Bon Kalindo yemwe wavekedwa unyolo mowilikiza pakatipa wati zithu zambiri ndizosokonekera m’dziko muno kamba koti dziko lino linapita kwa agalu.
Poyankhula mu pologalamu ya padera yomwe yaulutsidwa pa wayilesi ya Zodiak Lachiwiri madzulo, Kalindo wati atsogoleri onse omwe alamulirapo dziko lino anayesa kuyika patsogolo umoyo wa anthu zomwe ati pano sizikuchitika.
Iwo ati, “Nthawi ya Bakili Muluzi kunali starter pack, nthawi ya Bingu wa Mutharika kunali feteleza otchipa, nthawi ya Joyce Banda anayesetsa, Peter Mutharika nayenso anayesetsa kumbali yake. Nthawi imene ija mafuta a galimoto anali pa mtengo otsikilako koma awawa akuoneka ngati anali pa ludzu nthawi yaitali.
“Khoswe akamaluma munthu amapepelera munthuyo osadziwa kuti akulumidwa, koma awawa eee! Ndikufuna ndibwerezenso mopanda mantha; dzikoli lapita kwa a galu ndipo panakakhala mwayi woti anthu asamuke, m’Malawi muno mukanatsala a Chakwera okha ndi abale awo, ambiri akanasamuka chifukwa akuvutika.”
Mkuluyu wati amayembekezera kuti chipani cha Malawi Congress (MCP) chipanga zodabwitsa pa zaka zisanu zoyambilira, zomwe ati sizikuchitika. Bambo Kalindo ati pano andale kukacha akumaganiza kuti kodi apanga ndalama zingati zoti azitumize kunja.
Kalindo wadandaulanso kuti pansi pa ulamuliro wa MCP ndalama ikusowa kwambiri m’dziko muno zomwe wati zapangitsa a Malawi ochuluka kukhala pa umphawi wa dzaoneni pamene atsogoleri andalewo akulemera mododometsa.
“Munthu wakumudzi amangofuna akhale pa ntchito akhale pa bizinezi yabwino, koma andalewa amapanga dala ndi kuyamba kusowetsa ndalama monga m’mene apangira awa a MCP asowetsa ndalama m’dziko muno kuti anthu adzipita kwa iwo kukawapempha kuti iwo adzioneka ngati ndi milungu,” watelo Kalindo.
Kalindo anayankhula mokuluwika ponena kuti atsogoleri anzeru amatenga mafupa ndikumupatsa a galu kuti iwo azidya bwino minofu, ndipo ati nzodabwitsa kuti kuno andale akudya mafupa ndi minofu yomwe okha, kuwasiya anthu ali pa dzuwa.
0 Comments