
Mtsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) a Dalitso Kabambe ati zomwe achita apolisi powonelera anthu achiwembu akumenya mwankhanza anthu ochita ziwonetselo zachotsa chikhulupiliro cha aMalawi pa apolisi awo.
Iwo ati wamkulu wa apolisi mdziko muno a Merlyne Yolamu komanso nduna ya zachitetezo cha mdziko a Ezekiel Peter Ching’oma akuyenera achotsedwe ntchito mwansanga.
A Kabambe ati nkhanza zomwe achita anthu mu mzinda wa Lilongwe zawonetseratu kuti zinachita kukonzedwa kuti zipeleke chiwopsezo kwa nzika za dziko lino kuti zisamachite ziwonetselo zomwe ndi ufulu omwe uli m’malamulo aakulu a dziko lino.
Polankhula pa msonkhano wa atolankhani dzulo mu mzinda wa Blantyrre, a Kabambe ati demokalase mdziko la Malawi ili pa chiwopsezo ndipo apempha mabungwe akunja kuti alowelelepo.
“Boma lisiye nkhanza za mtundu uwu tsopano ndipo ateteze nzika zake, Malawi akuyenera mtendere, chilungamo ndi ufulu odzilamulira ndipo tikupempha tonse kuti tichilimike pa zimenezi ndi kupeza onse olakwa kuyankha pa nkhani zomwe alakwitsa,” atero a Kabambe.
M’modzi mwa omwe amatsogolera nawo ziwonetselo mu mzinda wa Lilongwe dzulo, a Sylvester Namiwa amenyedwa modetsa nkhawa ndi kuvulazidwa ndi anyamata a dzikwanje koma apolisi akungowonelera.
Bungwe la Citizen for Credible Elections (CfCE) ndi lomwe linakonza ziwonetselo zomwe zimachitika mu maboma angapo kuphatikiza Blantyre, Lilongwe, Mangochi ndi Mzuzu ndi cholinga chokakamiza wapampando wa bungwe loyendetsa chisankho a Annabel Mtalimanja limodzi ndi mkulu wa bungweli, a Andrew Mpesi kuti atule pansi ma udindo awo.
Gululi lati lapeleka masiku asanu ndi awiri kuti adindowa asiye ntchito yawo ndipo ati akapanda kutelo achita zinthu zina zomwe sananene.
0 Comments