Malawi News

Nzika ya ku Britain yabedwa ku Lilongwe

Nzika ya ku Britain yabedwa ku Lilongwe

Apolisi munzinda wa Lilongwe atsimikiza kuti nzika ya m’dziko la Britain ya zaka 26 yabedwa ndi anthu osadziwika pomwe imachokera ku mapemphero Lolemba masana. 


Malingana ndi ofalitsa nkhani za polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu, nzika ya ku Britain-yi yazindikilidwa ngati a Muhammad Kasman, omwe ndi m’modzi mwa akuluakulu ogwira ntchito ku Universal Industries.


Chigalu wauza nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko muno kuti, “Kasman amayendetsa galimoto la mtundu wa Toyota Fortuner CP 10842 ndipo akuyenda adakumana ndi anthu ena omwe amaguza ngolo zija amaguza anyamata ntauni.


“Anyamata a ngolowo anamutchingira mseu ndipo atatuluka kuti afunse kuti chikuchitika ndi chani, anthuwo anamugwira nkumuponya mu galimoto ya mtundu wa Noah, nkuthawa naye.”


Pomwe kafukufuku ofuna kupulumutsa Kasman adakali mkati, apolisi ati pano apeza lamya ya m’manja ya mtundu wa iPhone ya a Kasman koma akana kutchula dera lomwe ayipezela posafuna kusokoneza kafukufuku wawo.


Izi zikubwera pomwe pa 10 July 2024 munthu wina yemwe akuganizilidwa kuti atha kukhala ochokera m’mayiko aku Europe kapena Asia adapezeka atafa ku Ginnery Corner munzinda wa Blantyre, ndipo apolisi adati akukhulupilira kuti munthuyo adachita kuphedwa.