Malawi News

Julius “Chisyene Mesi” Paipi wabwelera ku DPP

…UTM yati yalemekeza chiganizo cha a Paipi popeza ndi ufulu wawo…


Patangopita masiku ochepa atalengeza kuti atuluka mchipani cha UTM, yemwe anali gavanala wa chipanichi m’chigawo cha kum’mawa, Julius “Chisyene Mesi” Paipi, wabwelera ku chipani cha Democratic Progressive (DPP).


Poyankhula Lamulungu pa msonkhano omwe akuluakulu a chipani cha DPP anachititsa m’boma la Mangochi motsogozedwa ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi mchigawochi, Bright Msaka, a Paipi anati atadya mutu komanso kudziguguda pa chifuwa awona kuti ndi chipani cha DPP chokha komanso mtsogoleri wake, Arthur Peter Mutharika, omwe ali ndi masomphenya otukula dziko lino.


Koma poyankhula ndi Malawi24 Lolemba mamawa, mkulu ofalitsa nkhani ku chipani cha UTM, Felix Njawala, wati chipani chawo chikuwafunira zabwino zonse a Paipi.


Kudzera mu uthenga wa pa lamya ya m’manja, a Njawala anati: “Tikuwafunira zabwino zonse. Iwo apanga chiganizochi molingana ndi ufulu wawo.”


Pa msonkhano-wu, anthu ena omwe anali ndi maudindo mchipani cha United Democratic Front (UDF) atulukanso mchipanichi ndipo alandilidwanso ku DPP.


Iwo akuti achita izi atamva mphekesera zoti chipani cha UDF chikulingalira zopanga mgwirizano wa chisankho ndi chipani cha Malawi Congress (MCP), zomwe akuti sizinawasangalatse.


Dziko lino likuyembekezeka kuchititsa chisankho chachikulu chosankha mtsogoleri wa dziko, aphungu a kunyumba ya malamulo komanso ma khansala pa 16 September chaka chino.