Ubale wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) ndi United Democratic Front (UDF) watekeseka ndipo atsirana mphepo pomwe mtsogoleri wa chipani cha UDF Atupele Muluzi watsindika kuti a Peter Mutharika akula ndipo akuyenera akapume.
A Muluzi anayankhula mawuwa pa msonkhano m’boma la Machinga, pomwe ati dziko la Malawi silikuyenera kubweleranso m’mbuyo, ndipo kuti a Mutharika akula akuyenera akapume.

“A Malawi sitikuyenera kubweleranso m’mbuyo, ine a Mutharika ndimawalemekeza koma akula akapume, nthawi ino ndi ya achinyamata,” anatelo Atupele Muluzi.
Mawuwa sanakondweletse chipani cha DPP chomwe oyankhulira chipanichi Shadrec Namalomba wati mawu omwe ayankhula a Muluzi ndi amtopola ndipo amangoyenera kuti apite ku misonkhano kukadzigulitsa okha osati kumakamba za nyumba ya DPP.
A Namalomba ati anthu anasiya kuwakhulupilira a Muluzi chifukwa ndi munthu yemwe sadziwa ndale ndipo amangowoneka mu nthawi ya chisankho chokha basi.
“Kodi a muluziwo ndi ndani kuti akayankhule za DPP, ndi ndani iwowo?” Anatelo a Namalomba m’chizungu.
Pa masankho a m’chaka cha 2020, a Peter Mutharika adasankha Atupele Muluzi kukhala yemwe ayende naye kupita ku masankho mu mgwirizano omwe awiriwa anagwamo koma sunaphule kanthu pomwe anagwa pamaso pa mgwirizano wa zipani 9 wa Tonse.
M’modzi mwa olankhulapo pa zochitika yemwenso ndi katswiri pa ndale Wonderful Mkhutche wati zikuwonetseratu makaka amene akuwonetsa a Muluzi akukonza njira yofuna kupanga m’gwirizano ndi a Lazarus Chakwera a chipani cha Malawi Congress (MCP).
A Peter Mutharika, Atupele Muluzi ndi a Lazarus Chakwera onse akatenga zikalata ku bungwe la MEC zofuna kupikisana nawo mu masankho a mu September.
0 Comments