Wachiwiri kwa mtsogoleri was dziko lino a Micheal Usi ati mipingo ikuyenelera osalema kupemphelera atsogoleri komanso ndi adindo onse kuti asamatengeke ndi zinthu kuyiwala chomwe analumbira kuti adzachitira anthu uku atagwira baibulo kapena Quran.
A Usi amayankhula izi ku Malamulo m’boma la Thyolo lero pamene anakakhala nawo pa mapemphero a tsiku lasabata.
M’mau ake wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikoyu wati ma udindo ena mdziko ndi m’mabungwe umakhala pafupi ndi zokuyesa zambiri koma chofunika ndi lumbilo lomwe unalumbira
A Usi omwe anagwiritsa ntchito nthano ya m’baibulo yokhudza otumidwa kukatenga Bulu, Iwo anati okatenga bulu sadamukwere pobwera naye kwa Yesu chifukwa anachita kutumidwa, Iwo ati izi mchimodzimodzi ndi adindo m’boma kuphatikiza iwo ngati wachiwiri kwa mtsogoleri komanso ndi adindo m’mabungwe.
Potsiliza iwo anati pa udindo wawo sadzachita zinthu zosemphana ndi kutumidwa ponena kuti mulungu ndi wadongosolo kuwaika iwo kukhala wachiwiri kwa a Lazarus Chakwera omwe ndi okonda Mulungu komanso malemu a Saulos Klaus Chilima omwe nthawi zonse sanachoke pa Mulungu kufikira imfa yawo.
Iwo anapemphanso mipingo kuti mwapadela idzipemphelera mkazi wa yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko mayi Mary Chilima.
0 Comments