By Wongani Mkandawire
Bambo Mphatso Augustine Sambo, amene pa nthawi ya mulandu wazisankho za 2019 umayimbidwa anali imodzi mwa mboni za Lazarus Chakwera, lero mu chaka cha 2024 ndiwo amene Mlembi wamkulu wa bungwe loyang’anira kalembera wa unzika la NRB – pamenenso ntchito za bungweli zikuyang’anidwa mwa chidwi makamaka mmene likulephelera ntchito yopereka ziphatso za unzika kwa a Malawi amene akuyenera kudzatenga nawo gawo pa zisankho za chaka cha mawa.
Chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga ndi msonkhano wa atolankhani umene zipani za DPP, UTM ndi AFORD zinayitanitsa lero ku Lilongwe, kumene mwa zina, zipanizi zadzudzula kukondera ndi kulephera kwa ntchito kumbali ya bungwe lopereka ziphatso za unzika – zimene zithandizire kuti a Malawi akwanitse kulembetsa mu kaundula wa zisankho za 2025.
Imodzi mwa mfundo zimene zipanizi zapempha kuti bungwe loyendetsa zisankho lichite ndi kuti bungweli ligwire ntchito ndi bungwe lopereka ziphaso zaunzika, ndipo paliponse pamene pakuchitika kalembera wazisankho, a NRB adzikhala pomwepo kulembetsa anthu oyenera ngati nzika – monga mmene zinachitikirapo mu 2019.
Potsutsana ndi ganizo la zipanizi, mlembi wamkulu wa bungwe la NRB wakana zokuti bungwe lawo lidzigwira pamodzi ndi bungwe loyendetsa zisankho ati ponena kuti ntchito zawo ndizosiyana.
Koma ofotokozera nkhani za ndale ena adabwa ndi kukana kwa a Mphatso Sambo, potengera kuti ntchito yolembetsa nzika komanso namawalemba mu kaundula wa zamasankho mabungwe awiriwa anachitirapo limodzi m’chaka cha 2019.
Kafukufuku wapadera waulura kuti kaganizidwe ka bambo Sambo sikodabwitsa kwenikweni potengera kuti iwo atha kukhala kuti akuyankhula motsutsana ndi zipani zotsutsa pofuna kusangalatsa President Chakwera amene anawasankha ngati mlembi wamkulu ku bungwe la NRB ngati cholowa chawo atatha kuyima mubwalo la milandu ngati imodzi mwa mboni za a Chakwera pamene mulandu wazamasankho a 2019 umayimidwa.
Mboni inanso imene a Chakwera anayithokoza poyipatsa ntchito ndi bambo Daud Suleman amene anapatsidwa udindo ngati mkulu woyendetsa bungwe loyang’anira ntchito za mawayilesi komanso makampani a mafoni, lija la MACRA.
0 Comments