Malawi News

A Mutharika ndi a Kabambe sadakatengebe ma pepala ku bungwe la MEC

Atsogoleri a zipani za Democratic Progressive (DPP) ndi United Transformation Movement (UTM) ndi ena mwa atsogoleri amene sadakatengebe zikalata zawo zowonetsa chidwi kuti apikisana nawo mu masankho amene akubwera a pa 16 September.


Malinga ndi ma lipoti, a Peter Mutharika alipira kale ndalama yawo yokwana 10 million Kwacha koma sadakatenge ma pepala awo.


Malinga ndi bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), pofika kumathero a sabatayi, atsogoleri asanu ndi atatu (8) ndi omwe atenga zikalata zawo zowonetsa kupikisana nawo (Nomination papers).


Malinga ndi MEC, omwe atenga zikalata ndipo alipira ndalama yokwana 10 million Kwacha ndi monga; Milward Tobias ndi Adil James onse oyima pawokha, a Lazarus Chakwera a MCP, Kondwani Nankhumwa a PDP, Kwame Bandawe a Chipani cha AAA, a Joyce Banda a PP, Atupele Muluzi a UDF ndi a Reverend Hardwick Kaliya oyima pawokha.


Bungwe la MEC lidzasiya kulandira zikalata za Nomination pa 5 July 2025.


Abusa a Hardwick Kaliya ndi okhawo omwe anatenga zikalata zawo kumathero a Sabatayi.