Malawi News

Kenani ayamikira boma kamba kachitukuko cha nseu

Kenani ayamikira boma kamba kachitukuko cha nseu

Kwa nthawi yaitali nzinda wa Lilongwe wakhala ukutchedwa ‘nzinda wa fumbi’ kamba koti uli ndi misewu ya fumbi koma pano, fumbi litha kukhala mbiri yakale kamba koti boma likumanga misewu mu nzindawu.


Kudzera patsamba lawo la m’chezo, a Onjezani Kenani ati tsopano nzinda wa Lilongwe ukuoneka bwino chifukwa chakumangidwa kwa misewu imeneyi ndipo iwo ati ndi onyadira kamba ka ntchito yotamandikayi.  


Onjezani Kenani
Kenani: Zili bwino

“Well done to the government for this beautiful road. Lilongwe has worn a new face. We didn’t like the last few years of clouds of dust, but joy comes in the morning,” atero a Kenani mchingerezi.


Posachedwapa, a Kenani anathandiza kusonkhetsa ndalama ndicholinga choti athandize oyimba otchuka a Paul Banda, omwenso ndi mchimwene wawo wa malemu Lucius Banda, pa nthenda yomwe ikuwasautsa ya ipsyo.