Malawi News

Engineer Mumba walumira mano ndipo wanenetsa kuti: “Ndikuyima ndipo ndikapambana!”

Engineer Vitumbiko Mumba walumira mano ndipo wanenetsa kuti iyeyo sanaluzepo zisankho choncho pa 8 August pano akayima ndikukatenga mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha MCP.

Mumba

Iyeyu, poyankhula ndi kanema wa Times usiku wathawu, watemesa nkhwangwa pa mwala kuti palibe chikuwaopsa kuti chingawagwetse osatenga udindowu.

“Chipani cha MCP chikufunika wachiwiri kwa mtsogoleri  wachinyamata yemwe angakwanitse kuthamanga ndi masomphenya a chipanichi, ndipo munthuyo ameneyo ndiineyo,” atero Mumba.

Iwo ati masomphenya awo ndi oti agwire ntchito yotukula dziko lino komaso chipani cha MCP mpaka pomwe angathere mtsogoleri wa chipanichi Lazarus Chakwera.

Anapitilizanso kuti akangopambana chisankhochi awonetsetsa kuti chipani cha MCP chikhale ndi njira zopangira ndalama zomwe ati ndikuphatikizapo kuyambitsa makampani a chipani. Iwo ati izi zitha kupititsa chipani cha MCP patsogolo.

Pa nkhani yopeleka ndalama kwa ma “delegates,” Mumba wavomela kuti akumapelekadi ndalama. Iye wati sangalore kuti anthu omwe akukumana nawo azibwelera kwawo chimanjamanja pomwe amakhala anthuwo awononga ndalama monga ya transport.

Pa nkhani ya kuchita bizinezi ndi mwana wa mtsogoleri wa dziko lino Nickson Chakwera, Mumba wati awiriwa samachita bizinezi limodzi ngakhale kuti wavomera kuti Nick ndi nzawo.

Iwo anenetsa kuti sakukhudzidwaso ndi kontalakiti ku Immigration yopanga ziphaso zoyendera. A Mumba anenetsa kuti iwo sakupanga bizinezi iliyonse yomwe anayipeza kamba kakucheza kwawo ndi mwana wa mtsogoleri wa dziko linoyo. Apa anenetsa kuti alibe ma “connection” ku nyumba ya boma.

Sharing is caring!