Malawi News

Anjatidwa kamba kogulitsa zipangizo za ulimi

Anjatidwa kamba kogulitsa zipangizo za ulimi

A Polisi ku Mchinji anjata abambo awiri powaganizira kuti amagulitsa zipangizo za ulimi zomwe anatenga pangongole ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited.


Malingana ndi bungwe la NEEF, abambowa ndi a Richard Banda komanso Charles Peter omwe ndi mamembala a gulu la Kamwendo Traders ochokera m’mudzi mwa Kamwendo Mfumu yaikulu Zulu m’boma la Mchinji


“Anyamatawa ndi mamembala a gulu la Kamwendo Traders ndipo alipo mamembala asanu ndi m’modzi. Iwowa anafunsa ngongole ya zipangizo za Ulimi ku bungwe la NEEF ndipo adapatsidwa feteleza matumba makumi atatu (30) ngati gulu.


“Bungwe la NEEF litamva zakugulitsidwa kwa matumbaku silidalekerere koma kuthamangira kumaloko komwe matumba ena alandidwa ndipo anyamatawa atsekeredwa mchitokosi ndipo auzidwa kuti abweze ngongole yomwe adatengayo,” latero bungwe la NEEF kudzera pa tsamba lake la mchezo.


Pakadali pano bungwe la NEEF lapempha anthu amene akutenga ngongole ya mtunduwu kuti asagulitse chifukwa kutero ndikusemphana ndi mgwirizano omwe adapanga ndi bungwe la NEEF ndipo wopezeka akugulitsa ayimbidwa mulandu.