Malawi News

Opikisana 13 pa President ku Malawi ndi chibwana chabe – Chaima

Opikisana 13 pa President ku Malawi ndi chibwana chabe – Chaima

M’modzi mwa akatswiri ozukutapo pa ndale a George Chaima ati m’mene dziko la Malawi lilili nkukhala ndi atsogoleri mpaka khumi ndi atatu (13) okapikisana pa mpando wa utsogoleri wa dziko ndi chibwana chabe chomwe Malawi akuwonetsa.


A Chaima ati nzodziwikiratu kuti zipani zina ngakhale oyima pawokha kumene sangasankhidwe ndipo ambiri mwa iwo angokhala odzikonda, oyang’ana zinthu zowapindulira ndinso dyera, ponena kuti dziko la Malawi limafunika atsogoleri a mphamvu ochepa okha kuti apikisane.


Poyankhula mu program ya The views Triangle” ya pa wayilesi ya Zodiak, a Chaima ati kuchulukana kwa opikisana kudzangopangitsa kuti dziko lino liwononge ndalama popangitsa masankho kachiwiri.


A Chaima komanso a Benedicto Kondowe atinso migwirizano ya ulendo uno ikhala yolowamo mwa mantha maka potengela kuti mu mgwirizano omwe unali wa chipani cha Malawi Congress Party MCP ambiri anatulukamo okhumudwa kale.


Iwo ati ngati pali kuthekera kopanga mgwirizano ena akuyenera adzichepetse ndikupeleka mphamvu kwa amene akhonza kutsogolera mgwirizano wa a mbali yotsutsa pano ndipo aliyense asamati atsogolera zomwe zikusodyeza dyera.


Benedicto Kondowe mkulu wa bungwe la Civil Society Education Coalition CSEC, wati zipani monga zotsutsa zikuyenera zitengerepo phunziro pa kukhala kwake kunja kwa boma ndipo zisadzayike Malawi kukhala opanikizika ngati zitapambana pa masankho.


Pa mndandanda wa omwe akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino akwana asanu ndi atatu malingana ndi bungwe la Malawi Electoral Commission MEC.


Pa onse omwe anakatenga zipepala ndi kupeleka ndalama yawo yokwana 10 million kwacha, anayi mwa iwo ndi omwe akufuna kudzayima pawokha pa mpando wa mtsogoleri.