Malawi News

“Ndalama zanuzo sungani,” abanja la Lungu akukanitsitsa thandizo la boma pa maliro

Madzi achita katondo m’dziko la Zambia pomwe akubanja la malemu Edgar Lungu akanitsitsa kulandira thandizo kuchokera ku boma ponena kuti bomalo linakanika kumuthandiza m’bale wawo ali moyo.


Mwazina, boma la Zambia likufuna liyendetse mwambo komanso lipeleke ndalama kuti zithandize pa mwambo wa zovutazi kuphatikizapo kunyamula thupi la malemu Lungu kochokera m’dziko la South Africa, ganizo lomwe likuoneka kuti liwomba mgolo.


Malingana ndi kanema wina yemwe taona, akubanja la Lungu atemetsa nkhwangwa pa mwala kuti salandira thandizoli ponena kuti boma linakanika kuthandiza m’bale wawo pomwe anali moyo. Iwo akuti boma silidathandize Lungu kupita kunja kukalandira thandizo pomwe amadwala.


Akubanja akuti “Edgar Lungu adapita yekha kuchipatala ku South Africa ndipo pobwelera mumusiye abwelerenso yekha. Inu aboma chitani zomwe muchitazo koma ife zisatikhudze.


“Ife tikufuna kulira munthu wathu, ndi munthu wathu tidzalira tokha. Taimabe pamawu athu oyamba oti palibe munthu adzatipatsa malo ena, ayi sitifuna,” watelo m’modzi mwa akubanja yemwe amayankhula ndi atolankhani komanso khwimbi la anthu omwe adasonkhana.


Munthuyu wati ngakhale pakufunika ndalama zankhaninkhani kuti zithandizire kuyendetsa mwambowu, iwo salandira thandizo lililose kuchokera ku boma.


“Ndauzidwa kuti zakudya zatsala zochepa, palibe vuto. Tikupempha akufuna kwa bwino kuti atithandize, ngati nkugona ndi njala tigona ndalama zawo asunge,” adaonjezera wakubanjayo.


Pakadali pano zikumveka kuti mbali ya boma ndi akubanja akokerana m’kachipinda komata komwe akukambirana kuti athetse kusagwirizana komwe kulipoku.


Edgar Lungu yemwe adabadwa pa 11 November, 1956, wamwalira pa 5 June, 2025 pa chipatala china m’dziko la South Africa komwe adapita kukalandira thandizo.