Malawi News

Mshomoli akodza usipa

Mshomoli akodza usipa

Zina ukamva kamba anga mwala! Lachitatu kudali chiphwete chosakanikirana ndi chisoni pa msika wa Sumbi ku Monkey Bay m’boma la Mangochi pomwe mkulu wina amakodza usipa chifukwa choswa mtedza ndi mkazi wa mwini.


Malingana ndi wailesi ya Dzimwe, pa 28 March, 2025, njondayi itamva kutentha mthupi, idakakhuthulira ukali wake wonse pa mayi wina ku Makanjira yemwe nayeso adali ndi ludzu losasimbika kamba koti wochita naye chipako ali kuulenje ku South Africa.


Mphuno salota! Njondayi siidadziwe kuti mwini munda adakonza nthiti yakeyo asadachoke. Patadutsa masiku ochepa chichitileni ubatizowo, mkuluyu adali ndi mantha othetsa mankhalu kuona ku “Malawi kwake,” kukuoneka zachilendo.


Mwazodzetsa tsemwe zina, gadafi wake adafufuma ngati buluzi womeza chule, ndipo akafuna kutaya madzi mkuluyu amatulutsa nsomba za mtundu wa usipa m’malo mwa madzi amchere aja. Poti womva m’mimba ndiye atsekura chitseko, Lachitatu mkuluyu adafika pa nsika wa Sumbi kukafunsa nzeru.


Koma paja mbuto ya kalulu idakula ntadzaonani, kumeneku khwimbi lidamuunjilira mkuluyu: ena kumumvera chisoni, pomwe ena amamunyogodola amvekere, “takodzani fada ife tikufuna usipawo,” kuiwara kuti akuba ndi ambiri koma kusagwidwa.


Mthengo mudalaka njoka! Atathandizidwa ndi akufuna kwa bwino, mkuluyu yemwe pano zeru ndi zina sadachite zengerezu koma kuwuyamba wobwelera kumpanje ku Phalombe komwe akusimba za malodzawa.