Malawi News

Liverpool zake zada

Liverpool zake zada

Anyamata awiri a timu ya Liverpool Darwin Nunez ndi Curtis Jones ndi omwe anambwandilitsa ma penate awo m’manja mwa goloboyi wa PSG Gianluigi Donnarumma pa bwalo la Anfield usiku wathawu mu mpikisano wa UEFA Champions League (UCL). Liverpool yatuluka mu mpikisano ndi kukankhira PSG ku ndime ya ma Quarter final.


Liverpool yatsanzikira Champions League pakhomo kutsatira chigoli chomwe Paris Saint-Germain (PSG) inapeza kudzera mwa Ousmene Dembele kuti masewelo athere (0-1) ndi (1-1) pa aggregate.


Liverpool inagoletsa penate imodzi yokha kudzera mwa Mohamed Salah pomwe Vitinha, Goncalo Ramos, Dembele, Desire Doue ndi omwe anagoletsela PSG kuti zithele (1-4) pakutha pa mphindi zonse 120+.


Mohamed Salah analira usiku wathawu kuona timu yake ikutuluka maka poganizira kuti wasemphana ndi UCL pamene contract yake ikunka kumapetonso chaka chino ndi timu ya Liverpool ndipo sizinadziwike ngati ayitanulebe contract yake.


Bayern Munich yadya Bayer Leverkusen 2-0 kudzigulira malo ku ndime ya quarter final ya UCL ka chi nambala 35 chibadwireni timuyi pomwe Barcelona yawamba Benfica 3-1 ndipo Intermillan yakomola Fayenoord 2-1.


Zonse zatha motere usiku wathawu;
⚽Barcelona 3-1 Benfica
⚽ Liverpool 0-1 PSG
⚽ Leverkusen 0-2 Bayern
⚽ Intermillan 2-1 Feyenoord