Malawi News

Katswiri wayikira ku mbuyomu Inkosi Gomani 5 pokapezeka ku Lunjika turn-off

Akatswiri olankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana ayikira kumbuyo ganizo la Inkosi Gomani 5 lokapezeka ku Lunjika turn-off m’boma la Mzimba pamodzi ndi m’tsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ku mwambo wokumbikira malemu Saulos Chilima ndi ena 8 omwe adafa pa ngozi ya ndege chaka chatha.


Kupezeka kwa Ngwenyama ku Lunjika turn-off sikudasangalatse anthu ena omwe amaganiza kuti mfumu ya Maseko Ngoniyi imayenera kukapezeka ku Nsipe komwenso kudali mwambo wina wokumbukira malemu Chilima.


Koma Augustine Mwandira yemwe amayankhula pa zinthu zosiyanasiyana, wayikira kumbuyo ganizo la Inkosi Gomani 5 ponena kuti zomwe adachitazi zasonyeza kukhwima nzeru komanso kuganiza kwa ngwiro.


“Sindikuonapo vuto kukapezeka komwe kudali mtsogoleri wa dziko lino, Chakwera, ndipo izi zangosonyezeratu kuti Inkosi Gomani 5 amaganiza mokhwima nzeru komaso kuti ndi mtsogoleri wa anthu onse,” watelo Mwandira.


Iye anapitiriza kufotokoza zakukhumudwa kwake ndi zina zomwe zidachitika ku mwambo wa ku Nsipe ponena kuti mwambowu udalowetsedwa ndale.


“Pomwe tikuyamika akubanja kamba kokonza mwambo wa mapemphero ku Nsipe, zidali zomvetsa chisoni kuti anthu ena kuphatikizapo atsogoleri a chipani cha UTM monga a Kaliati adatengerapo mwayi pa mwambowu ndikulowetsa ndale ndicholinga chonyoza boma zomwe ndi zinthu zosayenera,” adawonjezera Mwandira.


Pothirirapo ndemanga, katswiri winaso Tiyande Nyirenda wati potsatira kutulutsidwa kwa lipoti lokhudza ngozi ya ndegeyi, a Malawi sakuyeneraso kumalozanabe dzala koma kugwirana manja ndikuyendera limodzi kupita chitsogolo.


“Lipoti la BFU ya ku Germany, lafotokoza zoti ngoziyi idachitika kamba ka nyengo yoyipa komanso kusapanga chiganizo choyenera kwa womwe ankayendetsa ndegeyi, choncho ndikoyenera kuvomereza kuti palibe wina aliyense yemwe adapanga zaupandu kotero sibwino kupitiriza kulowetsa ndale pa nkhaniyi yomwe idakhudza mtundu wa Malawi.” Watelo Nyirenda.


Ena mwa anthu womwe adali nawo ku mwambo wa ku Nsipe ndi monga mtsogoleri wakale wa dziko lino Joyce Banda komanso mtsogoleri wa UTM a Dalitso Kabambe.