Malawi News

Aphunzitsi ochonga mayeso a Form 4 akunyanyala ntchito

Aphunzitsi ochonga mayeso a Form 4 akunyanyala ntchito

…akugonanso malo a nsikidzi…


Aphunzitsi omwe akuchonga mayeso a Form 4 ku St Mary’s Secondary School ku Zomba akunyanyala ntchito ati pofuna kukakamiza akulu akulu a MANEB kuti awapatse ndalama zawo zoyendera (transport) komanso ndalama zina zowonjezera.


Mmodzi mwa aphunzitsiwa yemwe sadafune kuti timutchule dzina wati Bungwe la MANEB silidawapatsebe ndalama zawo zomwe adayendera ndipo akufuna awapatse ndalamazi pamanja osati kudzera ku bank powopa kuwachotsera ndalama zina.


Iye watinso kupatula ndalama zoyendera zomwe akufuna, Iwo akufunanso Bungwe la MANEB liziwapatsa ndalama zapedera mofanana akagwira ntchito monga momwe amawapatsira anthu ena ogwira ntchito mothandizira kumaloko. 


Aphunzitsiwa atinso akufuna awawonjezere ndalama zomwe amawapatsa akachonga pepala lilinso lamayeso komanso akufuna aziwapatsa ndalama zamaphunziro (training) omwe amachita asadayambe kuchonga mayeso.


Iwo adandaulanso kuti malo omwe akugona ku St Mary’s Secondary School si abwino chifukwa akumalumidwa ndi nsikidzi.


Iwo atinso Bungwe la MANEB lidawapatsa mankhwala opopera udzuzu a Doom omwe ntchito yake yogwilira ntchito idatha kalekale zomwe zikuyika miyoyo yawo pachiwopsezo.


“Tikukhala ngati tili ku Ndende chifukwa tikugona malo ansikidzi komanso akumatipatsa zomwera tea zowonongeka,” anatero.


Iwo awopseza kuti apitilirebe kunyanyala kuchonga mayesowa pokha pokha atawapatsa ndalama zawo zomwe adayendera. 


Tidayesera kuti tiyankhule ndi ofalitsa nkhani za Bungwe la MANEB kangapo konse koma foni yake simapezeka.