Pentagon yati dziko la Amereka litumiza zida zina ndi ndege za nkhondo ku Middle East kuti zithandizire kuteteza Israel ku mtopola ulionse omwe dziko la Iran ndi maiko ena angachitire dzikolo.
Mkangano ukupitilirabe m’derali chifukwa cha kuphedwa kwa mtsogoleri wa Hamas Ismail Haniyeh ku Iran komanso wamkulu wa gulu la zigawenga ku Lebanon la Hezbollah.
Mtsogoleri wa Iran Ayatollah Khamenei wanenetsa kuti abwezera chipongwe chomwe Israeli yachita pa kupha Haniyeh.
Mtsogoleri wa Hamas adaphedwa ku Tehran Lachitatu pomwe anakakhala nawo pa mwambo olumbilitsa a Khamenei omwe angosankhidwa kumene ngati mtsogoleri wa dziko la Iran.
Iran ndi maiko ogwirizana nawo adadzudzula Israeli chifukwa cha chiwembuchi, koma dziko la Israel silinanenepo kanthu.
Haniyeh, wazaka 62, amatengedwa kuti ndi mtsogoleri wamkulu wa Hamas ndipo adatengapo nawo gawo lalikulu pazokambirana zomwe cholinga chake chinali kuthetsa nkhondo ya Gaza.
Imfa yake idabwera patangotha maola ochepa kuchokera pamene Israel idanena kuti idapha Fuad Shukr, mkulu wa asilikali a Hezbollah, ku Lebanon.
Magulu a Hezbollah ndi Hamas ndiovomerezeka pamaso pa dziko pa Iran.
0 Comments