
Njonda ziwiri ku Manja munzinda wa Blantyre, zabzala chinangwa kamba kochita chibwana cha mchombo lende kukonkha chakumwa choyankhulitsa chizungu ku mimba kukulira malikhwelu.
Malingana ndi wofalitsa nkhani ku polisi ya Soche, Aaron Chilala, Vincent Chotokoma wazaka 21, yemwe ankagulitsa nsapato ku Limbe, kumathero a sabata yatha adawonedwa akukonkha bibida ngati kulibe mawa chosecho akuti adali asadaponye ulimbitso m’mimba.
Thupi la Chotokoma yemwe adali wodya yekha lidapezeka lili lambaa kunyumba yake Lolemba lapitali m’mawa pomwe aponda apa nane mpondepo ake adamuyendera kuti akamuzonde.
Naye Steven Lizzi wa zaka 48, wa dera lomweli, bibida wamutsogoza ku ulemelero. Sabata yatha Lizzi adasemphana chichewa ndi achibale ake, ndipo pofuna kuchotsa nkhawa, iye adachoka pakhomopo ndikukayamba kuwutunga mwa mwauphikiranji.
Zotsatira zake, Lizzi adapezeka atatseka maso mphepepete mwa nsewu wopita ku nyumba kwake. Zotsatira zakuchipatala ndi zomwe zatsimikiza kuti mbiyang’ambezi zazima kamba kakumwa chakumwa chaukali asanadye.
0 Comments