Malawi News

A Joyce Chitsulo aikidwa m’manda

Misozi umakana kuwuma pomwe anthu amapelekeza thupi la yemwe anali wachiwiri kwa nduna ya zamaboma ang’ono ndi chitukuko cha kumudzi a Joyce Chitsulo kukaliyika m’manda dzulo kumudzi kwawo ku Thambani m’boma la Mwanza.


Ndi nkhope zawo zakugwa, manja ali kumbuyo misonzi ikukana kuwuma mazana mazana a anthu komanso adindo a boma kuphatikizapo mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera anali nawo pa mwambo opelekeza a Chitsulo omwe anamwalira Lachisanu lapitali atangogwa kunyumba kwawo mu mzinda wa Lilongwe.


Mkuyankhula kwawo nduna ya maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda ati mtsogoleri wa dziko lino anawona ukadaulo omwe a Chitsulo anali nawo ndi chifukwa anawasankha kukhala wachiwiri wawo posayang’anira makaka a chipani chawo.


A Chimwendo ati mu nthawi yonse yomwe anali ndi a Chitsulo zinawonetseratu kuti ndi mzimayi okonda dziko lake koposa, ndipo anali odzipeleka kuwona miyoyo ya anthu maka amayi, ikusintha.


Mwana oyamba wa a Chitsulo Maureen m’mawu ake pakulira anati mayi awo anali achikondi kwambiri ndi okonda banja lawo komanso ena adera.


Iye anayamika boma pa zonse zomwe anawachitila mayi awo, ndipo anatsutsana ndi nkhani zina zabodza kuti mtsogoleri wa dziko lino sanawathandize a Chitsulo kuyambira pomwe anapanga ngozi pomwe ankachokera ku Mzuzu.


Sipikala wa nyumba ya malamulo a Catherine Gotani Hara m’mawu awo anati a Chitsulo anali ndi ukadaulo wapaderadera, komanso analimbikitsa amayi ochuluka mnyumbayi komanso mdziko muno.


A Hara ati mboni zilipo zambiri pa momwe a Chitsulo amagwirira ntchito molimbika ku ma komiti a nyumba ya malamulo ngakhale ku dera lomwe amaliyang’anira.


Apo a Hara anayitana Joyce Chitsulo mwachisoni kangapo ndi kunena kuti adzamusowa kwambiri.


A Joyce Chitsulo anali mzimayi oyamba kukhala phungu ku dera la kumadzulo kwa boma la Mwanza, ndipo amwalira ali ndi zaka 47, iwo asiya mamuna, ana anayi ndi zidzikulu ziwiri komanso dera lawo la Phungu.