Malawi News

Zeze akuthawa Fada Moti – a Malawi ang’alura

Zeze akuthawa Fada Moti – a Malawi ang’alura

Pomwe namatetule wa chamba cha Amapiano, Zeze Kingston walengeza kuti zolandira ma “award” wasiyira ena, anthu ena ati uku nkuwopa kusambitsidwa chokweza ndi woyimba nzake Fada Moti yemwe wayaka moto.


Lachinayi, Zeze watulutsa kalata yofotokoza kuti sakufunaso kumasankhidwa m’mipikisano ya oyimba ofuna kulandira ma award ponena kuti walandira mphotozi zochuluka choncho nkwabwino kuti asaphangire, enaso alaweko ku zuna kwake.


Koma a Malawi ochuluka, makamaka m’masamba amchezo ali ndi maganizo osiyana; ambiri ati ndi bodza lankunkhuniza kuti Zeze akufuna kupeleka mwayi kwa oyimba ena ponena kuti woyimbayu wazidziwa kuti watha mtoto, ndipo wachita mwambi oti ukayipa dziwa nyimbo.


Munthu wina yemwe anayikira ndemanga za nkhaniyi pa fesibuku wati, “A Zeze musaname kuti mukufuna kupeleka mwayi kwa ena, ingonenani kuti Fada Moti sakubwera mocheza, akukupatsa mpishupishu.”


Anthu ena ati potengera ndi m’mene mayimbidwe ayendera chaka chino, Zeze naye wadziwiratu kuti sangaphure kanthu. “Koma kunena zoona chaka chino simukanaphura award iliyonse bwana,” wang’alura wina patsamba lathu la fesibuku.


Ngakhale ena akuti, anthu ena ochuluka ayamikira Zeze ponena kuti “Munthu odziwa kuvina amadziwaso yekha nthawi yotuluka m’bwalo,” ndipo ena akuti Zeze wawonetsa mtima osadzikundikira.


Chaka chatha, Zeze analandira mphoto ya oyimba wabwino komaso mphoto zina ziwiri ku Maso Awards komaso mphoto ya oyimba wabwino ku MBC Entertainers of the Year Awards.