Itatuluka mu ligi m’chaka cha 2023, timu ya apolisi ya Blue Eagles tsopano yabweleranso mu ligi yayikulu ya mdziko muno ya TNM Super League kutsatira kukhala akatswiri mu chikho cha Chipiku Stores Central Region Football League itagonjetsa Armour Battalion 4-1 pa bwalo la ADL ku Lilongwe Lachitatu.
Eagles yomwe yatsala ndi masewelo awiri kuti imalize masewelo ake onse a ligi ya mchigawo chapakati imangofunika point imodzi kuti ibwelere mu ligi yayikulu.
Zigoli za Lankeni Mwale, Maxwell Gustavo , Paul Master , Checkson Alinzi ndi Battalion inapeza chopuputira misonzi kudzera pa penate kuchoka kwa Lumbani Mkandawire zinali zokwanira pa tsiku la chimwemwe kwa Nkhwazi za ku Lilongwe ndi kuti zizitsogola ndi ma point 14.
Mphunzitsi wa timu ya Blue Eagles omwe tsopano sanagonje masewelo aliwonse, Elia Kananji wati masewelo aliwonse amawatenga kuti ndi masewelo ovuta ndipo wati mpira wa ku chigawo ndi owawa chifukwa ndi kowuma.
Blue Eagles ikutsogolera pa mndandanda wa ma timu a mchigawo cha pakati pomwe ili ndi ma points 54 kuchokera mu masewelo 20, kutsatilana ndi Villa FC yomwe imathamangira ma Eagle ndipo pakali pano ili ndi ma points 40 kutsatira kufanana mphamvu kwake ndi Namitete Zitha.
Blue Eagles yomwenso ndi akatswiri a chikho cha 2024 FDH bank cup abweranso mu ligi ya TNM kutsatira kupezeka kwa malo atatuluka ma timu atatu a Baka City, Bangwe All stars ndi FOMO ya ku Mulanje.
Zatelemu kwatsala timu imodzi ya mchigawo cha ku m’mwera kuti idzipezele malo ndipo ma timu atatu a Ekhaya FC , Red Lions ndi Bullets reserve ndi omwe ali ndi mwayi opeza malo mu ligi ya TNM ya mchaka cha 2025.
0 Comments