
Timu ya Silver Strikers yaswa akatswiri a Castel Challenge Cup a Mighty Wanderers mochita kuchokera kumbuyo kukafanana mphamvu 2-2 zomwe zinakusila awiriwa ku ma penate mu mpikisano wa NBS Bank Charity Shield dzulo pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.
Bob Mpinganjira wati timu yake yagonja mokhumudwitsa komabe anyamata ake asewera mpira wabwino kwambiri ndipo kutulutsidwa kwa m’modzi mwa osewera ake kunasokoneza.
Silver strikers yomwe yalanda ukatswiri kwa Bullets, inayamba mozizira pomwe inakanika kukakha kuti ipeze mpata wa chigoli kumayambiliro kwa masewelowa.
Oyamba kugoletsa anali Sama Thierry Tanjong pa mphindi ya chi 26 atatembenuka nkumenya bomba lomudutsa goloboyi wa Silver, George Chikooka.
Chigawo chachiwiri, osewela wakale wa Bullets Precious Sambani anapeleka mpira kwa Binwell Katinji yemwe analumikiza mpira kugagwedeza ukonde pa 55 kuti ikhale 1-1, asanabwere blessings Singini pa 68 kutsogoza Manoma.
Zebron Kalima anagwetselamo atalandira mpira kuchokera kwa osewela wakale wa blue Eagles McDonald Lameck kufananiza mphamvu 2-2 kukankhira masewelowa ku ma penate omwe athera 5-3 kukomera akatswiri a 2024 TNM Super League, ma Banker.
Mphunzitsi wa timu ya Wanderers Bob Mpinganjira wati anali ochepa chifukwa cha kutuluka kwa Chaziya koma anawonetsabe kuti ali ndi mphamvu.
Mphunzitsi wa Silver Strikers wati masewelowa anali abwino kwambiri, ngakhale anayamba udyo, koma wati masewelowa akwanitsa kupeleka mphamvu kwa osewera pomwe akukonzekera nyengo ya masewelo a 2025/2026.
0 Comments