Malawi News

Milandu ina ndi yongofunika kukambirana – Gangata

Milandu ina ndi yongofunika kukambirana – Gangata

Wachiwiri kwa mtsogoleri mchipani cha Democratic Progressive (DPP) mchigawo cha pakati, a Alfred Gangata, ati mchitidwe omangana wawonjeza pomwe ati amanganso Commissioner wa apolisi chifukwa cha paint. Iwo ati commissioner wa apolisi monga wamkulu samayenera kumumanga koma amangoyenera kumuitana kuti afotokoze m’mene zinakhalira ndipo abweze ngati anatengadi zinthu.


Polankhula mu program ya Times Exclusive usiku wa Loweluka, a Gangata ati sizimayenera kufika pomanga commissioner wa apolisi, ndipo ati ngati aMalawi tidzikhala m’maso (serious).


“Are you serious? kumanga police commissioner chifukwa cha paint? zinthu sizikuyenda bwino, mavuto amenewa professor akangoti wabwera adzawonetsetsa kuti aliyense agwire ntchito yake mmene amadziwira,” anatero a Gangata.


Posachedwapa bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti- Corruption Bureau (ACB) pa 24 March 2025 lidamanga a Richard Luhanga yemwe ndi commissioner wa polisi mchigawo cha ku mpoto chifukwa chogwiritsa ntchito ofesi yawo molakwika.


Malinga ndi mkulu ofalitsa nkhani ku ACB, a Egrita Ndala, kumangidwa kwa a Commissioner Luhanga kudatsatira kafukufuku yemwe adapanga ndipo adapeza kuti wamkulu wa apolisiyu adagwiritsa ntchito paint wa ku chipatala cha polisi ku mzuzu ndipo anagwiritsa ntchito paint-yu ku ntchito ya zofuna zawo mzaka za 2022 ndi 2023 pomwe adali commissioner wa apolisi.


Bungwe la ACB lidati a Luhanga adatenga paint yemwe bungwe la Press Trust Limited lidapeleka ku polisi kuti apemtele chipatala, ndipo iwo adakapentera zomanga zawo zomwe zili ku Nkhozo Estate ku Bolero.


Mu macheza awo a Gangata atinso apolisi ndi amodzi mwa omwe akuvutika kwambiri chifukwa amakhala akulandira malamamulo osakhala bwino ndipo ati apolisi akuvutika komanso akugwira ntchito mwa mantha.


“Ndinadwala ine usiku koma kumabwera ma orders kuti ameneyo asapite ku chipatala, tangoganizani munthu wadwala usiku nde muzidikira kuche?” anafunsa aGangata.


Posachedwapa a Gangata akhala ali bwenzi la zitolokosi za apolisi pomwe anawamanga koyamba pa mlandu owaganizira kuti adasema zikalata zabodza za ku bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA), ndipo kachiwirika adawamanga chifukwa chogwiritsa ntchito satifiketi ya folomu folo yomwe ati adaipeza mwachinyengo.