Mayi wakale wa fuko la Malawi a Gertrude Mutharika alangiza anthu m’dziko muno makamaka amai kuti pamene nyengo yokopa anthu mu chisankho cha chaka chino ikuyandikira, asakopeke ndi andale adyera amene amakhala kalikiliki kugawa katundu osiyanasiyana ndi cholinga choti azavoteledwe m’mipando yosiyanasiyana.
A Mutharika ayankhula izi Loweruka m’boma la Balaka kumene anali mlendo olemekezeka pa msonkhano wa amai achipanichi mchigawo cha kum’mawa omwe unachitikira pa bwalo la sukulu ya pulaimale ya Balaka.
Iwo anachenjeza azimai kuti akhale tcheru chifukwa mu nyengo yokopa anthu, kutulukira andale omwe cholinga chawo ndikungofuna kuwasocheletsa.
“Akakupatsani landirani.Ndipo akakupatsani idyani,” adatero a Mutharika.
Iwo anapilitizanso kulangiza anthu m’dziko lino kuti asadzabwelezenso chibwana chovotera mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera komanso chipani MCP ponena kuti alephera kuyendetsa dziko lino.
Ndipo m’mawu ake, wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawochi a Bright Msaka anati chibadwireni chawo, iwo sanaoneko mavuto ngati omwe nzika za dziko lino zikukumana nawo mu utsogoleri wa a Chakwera ndi chipani cha MCP ndipo anatsindika kuti a Chakwera alephera kukwaniritsa malonjezo omwe amkapanga asanasankhidwe kukhala mtsogoleri wa dziko lino.
A Msaka omwenso ndi phungu wa dera la Machinga Likwenu anati nthawi yakwana tsopano kuti aMalawi atuluke mu nsinga za umphawi povotera chipani cha DPP komanso mtsogoleri wake, Arthur Peter Mutharika.
Pothilirapo ndemanga pa momwe zinthu ziliri m’dziko muno, gavanala wa chipani cha DPP m’chigawochi a Daud Chikwanje anati dziko lino likudutsa mu nyengo yowawa kwambiri chifukwa cha mavuto adzaoneni otchedwa “Cyclone MCP” koma analimbikitsabe anthu kuti asataye chiyembekezo chifukwa posachedwapa, mavutowa akhala mbiri ya kale.
Pa msonkhanowu panafika atsogoleri a chipani cha DPP ochuluka kuchokera m’chigawochi.
0 Comments