

Nthumwi zayamba kufika ku Comesa Hall mu mzinda wa Blantyre komwe chipani cha People’s Development (PDP) chikuchititsa msonkhano wake waukulu.
Yemwe akugwilizira udindo wa mneneri wa chipanichi a Rhodes Msonkho wati nthumwi zokwana 1200 ndi zomwe zikuyembekezeka kufika pa malowa.

A Msonkho atinso aitana zipani zina ku msonkhanowu. Mamembala ena a chipani cha Peoples (PP) afika kale.
Mtsogoleri wa chipanichi a Kondwani Nankhumwa, omwe alibe opikisana nawo, akuyembekezeka kutsekulira msonkhanowu.
0 Comments