Malawi News

Kusowa kwa mafuta kukubweretsa chidani ndi mikangano

Kusowa kwa mafuta kukubweretsa chidani ndi mikangano

Usiku wathawu, monga zikukhalira ku Malawi, mizere masiku osowa mafuta ano, azibambo anatsala pang’ono kutsilana makofi pa malo omwetsela mafuta a Tengani Engen m’boma la Nsanje, pamene panalowa chisokonezo pa mizele ya anthu omwe anandandana kufuna kugula mafuta a galimoto.


Ntchito yomwetsela mafutayi inayima kwa mphindi zingapo omwetsa mafuta atanyanyala ndi kukangana kwakukulu komwe kunachitika ndi eni ma galimoto, njinga zamoto ndi ma venda ogula mafuta mu zigubu, anthuwa amalozana dzala kuti pakuyenda chinyengo ndi kukondera ndipo ati pali ka guru kena kochokera ku Mozambique komwe kakufuna kumagula mafuta mwachinyengo mu zigubu.


Malawi24 inali ili pa malopa kuyambira pamene chi galimoto chodzatula mafuta (tanker) cha mtundu oyera chinadzatsitsa Petrol wa ma litre pafupifupi 10,000.


Pa malowa panabwera bata atayika lamulo kuti galimoto lililonse lithile mafuta a ndalama zosapyola 50,000 kwacha.


Malawi24 inawona galimoto la mtundu wa Lole litanyamula zi ma tank za mtundu wa blue ziwiri kumbuyo ndipo linathira ma lita 400, komanso ma galimoto ena omwe amachita kutekesedwa kuli kunyanyira mafuta mu tank.


Si zobisa kuti m’malo omwetsela mafuta mukuchitika zinthu zambiri zomwe zikuika pa chiopsezo anthu ake ogwira ntchito komanso ngakhale malowo kumene popeza ndi malo amene ndi owopsa ndipo chilichonse chimayenera chichitike mosamala (safety cautions).


Monga zikukhalira m’malo ambiri omwetsela mafuta, malo amene tinaliwa panali njinga zambiri komanso zigubu za ma 5 ndi 20 lita zoletsedwa zili m’masaka zina m’manja,


Mkulu wa Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA), a Henry Kachaje adandaula kuti mavenda ndi omwe akupangitsa kuti mafuta asamakwanile m’dziko muno.