Malawi News

Kulibe chipatala cha Namiyasi ku Mangochi – Kingstone

Kulibe chipatala cha Namiyasi ku Mangochi – Kingstone

Phungu wa dera la pakati m’boma la Mangochi, Victoria Kingstone, watsutsa kwa ntu wa galu zomwe wanena mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera, kuti boma lamanga chipatala cha Namiyasi.


A Chakwera anafotokozera Nyumba ya Malamulo Lachisanu kuti pansi pa ulamuliro wawo amanga zipatala zing’onozing’ono 25 m’boma la Mangochi zomwe ndi kuphatikizapo chipatala cha Namiyasi.


Komabe, a Kingstone, kudzera pa tsamba lawo la Facebook ati ili ndi bodza lamkunkhuniza ponena kuti Chipatala cha Namiyasi kulibe.


“Dera la Namiyasi lili mu Mangochi Central ndipo Health post iyiyi kulibeko. Unless kulinso malo ena otchedwa Namiyasi kapena…tikufufuza ndithu. Koma Namiyasi wa ku Mangochi Central Health post iyiyi kulibe. Zikomo,” anatero a Kingstone.


Izi zikudza pomwe zadziwikanso kuti zina mwa ntchito za chitukuko zomwe a Chakwera anena kuti apanga m’madera osiyanasiyana ndi bodza chabe.