
Bungwe loyendetsa mpira wa miyendo m’dziko muno la Football Association of Malawi (FAM) kudzera mu komiti yake, lakana kuvomeleza ndi kuika pa mndandanda ma bwalo asanu mwa ma bwalo oti ayambe kugwiritsidwa ntchito pomwe masewelo a mpikisano waukulu wa TNM Super League akhale akuyamba m’masiku asanu akudzawa.
FAM kudzera ku mbali yake ya club licencing, yati m’mwezi wa January ndi March inaunikira ma bwalo 16, koma yavomeleza ma bwalo 11 okha omwe ali okwanira kuchititsa masewelo a mu mpikisano wa 2025/2026 super league, ndipo yayika pambali ma bwalo asanu.
Malinganana ndi FAM, ma bwalo a Aubrey Dimba, Civil ndi bwalo la Mpira ku Chiwembe, ayikidwa pa mbali kuti enuwake akonze mavuto ang’ono ang’ono kuti akhonzano kuwavomeleza. Pomwe ma bwalo a Balaka ndi Chitipa ati si okwanira konse kuchititsa masewelo.
Malinga ndi mkulu woyendetsa nkhani zopeleka zilolezo (Club Licensing Manager), Clement Kafwafwa, FAM yavomeleza ma bwalo monga, Bingu (Lilongwe), Kamuzu (Blantyre), Chitowe (Nkhotakota), champion (Dowa), Rumphi (Rumphi), Silver (Lilongwe), Nankhaka (area 30 Lilongwe), Dedza (Dedza), Mulanje (Mulanje), Karonga (Karonga) ndi Mzuzu (Mzuzu).
Kafwafwa wati anuwake a ma bwalo adauzidwa kuti akonze mavuto omwe anawonedwa pomwe FAM imayendera ma bwalowa koyamba m’mwezi wa January ndipo ati ena anakonza pomwe ena sanakonze mavuto a mabwalo awo.
“Tipitilira ndi kuwunika mabwalo kufuna kuwonetsetsa kuti zonse zofunika zikutsatidwa,” anatero a Kafwafwa mu kalata yawo.
Peter Fote m’modzi mwa akatswiri osakatula nkhani za masewelo mu program ya Sports 360 pa kanema wa Times wati FAM imayenera itulutse mabwalo mwachangu kuti ngati pali zofunika kukonza zikonzedwe mu nthawi yake.
FAM yatulutsa mndandanda wa ma bwalo Lolemba pomwe mpira wa mu mpikisano wa 2025/2026 TNM Super League ukhale ukuyamba Loweluka mabwalo osiyanasiyana.
0 Comments