Malawi News

Dan Lu watulutsidwa pa belo

Dan Lu watulutsidwa pa belo

Woyimba Dan Lu yemwe anawona ngati ku maloto pomwe anathilidwa dzingwe Lachiwiri munzinda wa Lilongwe, tsopano watulutsidwa pa belo.


Posatengera kugundika kwake potulutsa nyimbo zochemelera boma la MCP, apolisi adanjata Dan Lu pomuganizira kuti wavulaza ogwira ntchito ku bungwe logulitsa madzi munzindawu la Lilongwe Water Board (LWB).


Apolisi ya Lingadzi adati Dan Lu adamenya wogwira ntchito ku LWB-yu pa nthawi yomwe amafuna kudula madzi kunyumba kwake ku Area 49 kamba kosalipira ndalama malingana ndi dzuwali.


AMalawi analinkhwila mkuluyu atatulutsa nyimbo yake yotamanda mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ndi boma la MCP, yotchedwa ‘Kumenya Kugwetsa‘ kamba koti m’mene nyimboyi imatuluka nkuti anthu ambiri akudandaula ndi m’mene a Chakwera akuyendetsera dziko lino.