Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati lipoti la zotsatira za kafukufuku wa ngozi ya ndege lipelekedwe kwa maanja okhudzidwa pofika lero Lachisanu.
A Chakwera atinso kuyambira lolemba lipotili alitanthauzire mu zilankhulo zina za ku Malawi kuno kuti anthu athe kuwelenga.
Komiti yomwe mtsogoleri wa dziko lino adaisankha kuti ifufuze zonse zokhudza ngozi ya ndenge ndi kutayika moyo kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima limodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu ku Nthungwa m’boma la Nkhatabay inapereka lipotili kwa a Lazarus Chakwera dzulo ku Kamuzu palace mu mzinda wa Lilongwe.
A Chakwera ati ntchito yofufuzayi yayika pa mbalambamda omwe amafufuza ndipo nzosabisa kuti lipotili lawayika poyera ofufuzawa maka poti pali ena amene sangamvetsetsebe ndipo ena atenga izi kukhala zochitira ndale popeza ma bala a ngozi ya ndege sanapolebe.
Malinga ndi wapampando kwa commission-yi, Jabbar Alide wati akukhulupilira kuti lipotili lithandiza kuthunzitsa mitima ndipo ikhala mbali imodzi yotonthoza komanso kumanga Malawi wabwino.
Iwo ati kwa masabata asanu ndi awiri akhala akulandira, kuunika, ndi kuzukuta ma umboni onse amene anapeza kwa nathu okwana 133 kuchokera kwa anthu amene anawonekera ku Commission atalumbira kupelekera umboni owona.
Commission-yi imafufuza Ndege ya mtundu wa Donnier 228 202k MAF-TO3 yomwe inagwa pa 10 June ndi kupha anthu 9 pomwe ndegeyi inkapita ku Mzuzu.
0 Comments