Apolisi m’boma la Nsanje atsekera matate atatu mchitolokosi atapezeka ndi Nyanga ya Njovu yomwe anatangwanika kutsatsa kufuna kupeza msika.
Malinga ndi oyankhulira polisi m’bomali, a Agnese Zalakoma, omwe atsimikiza za nkhaniyi, atatuwa amangidwa nzika zakufuna kwabwino zitawatsina khutu kuti pali njonda zina zomwe zasowa msika wa Nyanga ya Njovu ndipo zikutsatsa katundu oyika anthu m’mavutoyu.
Malinga ndi a Zalakoma, apolisi ofufuza limodzi ndi atetezi a zakhalango anasaka athuwa omwe anawapeza ndi Nyanga za Njovu ziwiri.
Abambo atatuwa awavulitsa ma lamba a mchiuno ndi kuwakankhira mkachipinda kosadzadza kuyembekekezera kukayankha milandu yawo yopezeka ndi kugulitsa Nyanga ya Njovu zomwe ndi zosemphana ndi lamulo 86 losungira nyama zakutchire ndi zamkhalango.
A Zalakoma ati atatuwa ndi a Osman Osman a zaka 24, Dhino Alfred a zaka 27 onse ochokera m’mudzi mwa Nthukuso m’boma la Nsanje komanso a Daniel Namaliwa a zaka 25 ochokera kwa Mitambo kwa mfumu yayikulu Kaduya ku Phalombe.
0 Comments