Malawi News

Anjatidwa kamba ka umbava

Anjatidwa kamba ka umbava

Abambo awiri omwe ndi akabwerebwere a ku ndende akwidzingidwa ndi apolisi powaganizila kuti amaba katundu osiyanasiyana m’ma nyumba aanthu m’boma la Kasungu.


Malingana ndi wachiwiri kwa m‘neneri wa polisi ya Kasungu, Miracle Hauli, abambowa ndi a Eleson Nkhoma azaka 25 ndi a Thomas Mwale azaka 30 ndipo anagwirapo ukayidi m’mbuyomu.


A Hauli ati abambowa awapeza ndi  katundu osiyanasiyana yemwe anaba monga njinga ya kapalasa, kanema za Plasma, lamya zamakono zitatu, Home theater, solar battery, matumba aufa, mwazina.


Abambowa akaonekera ku khothi posachedwa kuti akayankhe mulanduwu.


A Eleson Nkhoma amachokera kwa Juma m’dera la mfumu ya ndodo Mwase pomwe Thomas Mwale amachokera kwa Chisazima m’dera la Suza.