
Masewelo ena aakulu lero lamulungu 4:00 masanawa pomwe Manchester City chindunji ndi makosana a Liverpool omwe pano akuyenda mapewa m’mwamba kutsogola ndi ma points awo 61, mu chikho chachikulu ku England cha English Premier League (EPL).
Pomwe masewelo ayake pa bwalo la Etihad, Nottingham Forest yalowera ku St James Park kukababadana ndi NewCastle.
Asanachitike masewelo a lero, chisakaziko chachitika dzulo loweluka ndipo chaphwanya mitima ya timu yomwe yakhala isakugonja m’masewelo pafupifupi 15 ya Arsenal. Onse limodzi ndi timu ya Chelsea awavwivwinyiza m’matope pomwe awumbudzulidwa mosayembekezereka, ndipo Manchester United inachita kuchokera kumbuyo modzandira kuti ipateko point imodzi itafananitsa mphamvu ndi Everton.
Mphunzitsi wa Arsenal Mikel Arteta anachita kunena kwa atolankhani kumeneko kuti “Ndine okwiya kwambiri” nde zokwiyilazo angadziwe ndi otsatira.
M’mene zatelemu, mawu oti “Arsenal imalimbikira koma zomwe imafuna m’moyo uno simadziwa” akhonza kuphelezera pomwe akupitilira kudzichulukitsila chi ntchito chofuna kuyipeza ndi kupitilira Liverpool pomwe ma points 11 ndi omwe alekanitse awiriwa ngati Liverpool ingapwine Manchester City kukamwa.
Masewelo onse loweluka
⚽ Everton 2-2 Manchester United
⚽Arsenal 0-1 West Ham
⚽ Bournemouth 0-1 Wolves
⚽ Fulham 0-2 Crystal Palace
⚽Ipswich 1-4 Tottenham Spurs
⚽ Southampton 0-4 Brighton
⚽Aston Villa 2-1 Chelsea
0 Comments