Malawi News

Zayang’ana kungolo, Calista agwa kuzisankho zachipulura

Zayang’ana kungolo, Calista agwa kuzisankho zachipulura

Yemwe anali mkazi wa mtsogoleri wa kale wa dziko lino malemu Bingu Wa Mutharika, Calista Chapola, akudziguguda pachifuwa pomwe wagwa chadodolido pa zisankho zachipulura m’chipani cha Malawi Congress.


Chapola adasamuka mchipani cha Democratic Progressive (DPP) chomwe adayambitsa amunake nkulowa United Transformation Movement (UTM). Poti pamodzimodzi padaoletsa dzungu, mayiyu adasamukanso ku UTM nkulowa chipani Malawi Congress (MCP) komwe maloto ake odzapikisana pa chisankho chaphungu wa Nyumba ya Malamulo asanduka a chumba.


Malingana ndi chikalata cha zotsatira chomwe tawona, Chapola yemwe pa chisankhochi adalembetsa kuti Calista Bingu, wapeza mavoti 196. Maria Nakwenda Kambuzi, ndi yemwe wasadabuza Chapola pamodzi ndi ena 8 omwe amapikisana. Kambuzi wapeza mavoti 485.


Zatelemu, Chapola ngati angakakamile kudzapikisana nawo pa chisankho chikubwerachi akuyenera kutulukanso MCP ndikulowa chipani china kapena kudzapikisana ngati phungu woyima payekha.