
Mtsikana wa zaka 15, Enifa George, wafa atawombedwa ndi mphenzi m’mudzi mwa Amoni 1, mfumu yaikulu Nsamala ku Balaka.
Inspector Gladson M’bumpha yemwe amayankhulira nkhani apolisi m’bomali watsimikiza izi poyankhula ndi Malawi24.
A M’bumpha ati ngozi-yi yachitika usiku wa Lamulungu, pa 31 March, 2025 ndipo panthawiyi kumagwa mvula yamphamvu ndipo chiphaliwali chitamenya chinamupeza mtsikanayu kuchipinda kwake komwe amagona ndipo adafera pompo.
Iwo atinso madotolo a pa chipatala chachikulu cha Balaka ataliyeza thupili adapeza kuti malemuwa amwalira kaamba ka mphamvu ya nyesi ya magetsi yochokera ku mphenzi.
Malemuwa amachokera m’mudzi mwa Yosefe, mfumu yaikulu Ganya m’boma la Ntcheu.
0 Comments