Malawi News

Papa Francis wadwalika

Papa Francis wadwalika

Akuluakulu a mpingo wa Katolika ati mtsogoleri wawo pa dziko lonse, Papa Francis wadwalika zedi.


Kudzera mu kalata yofotokoza zaumoyo wa papa Francis, ofesi yofalitsa nkhani ya Holy See, yati Loweluka zinthu sizinali bwino pa mtsogoleri wawoyu yemwe akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Gemelli mu nzinda wa Rome.


Kalatayi yati m’mawa wa loweluka, Papa Francis amavutika kwambiri kupuma zomwe zidapangitsa kuti afunikire kukhala pa makina othandizira kupuma.


“Papa amafunikiranso kupatsidwa magazi. Ali tcheru ndipo tsiku lonse latha ali pampando, ngakhale kuti ali pa ululu waukulu kuposa dzulo,” yatelo kalatayi.


Papa Francis adagonekedwa pa chipatala cha Gemelli Lachisanu sabata yatha kamba ka nthenda ya chibayo yomwenso idakhudza mapapo ake. Lolemba sabata ino, nthendayi idakula kupangitsa kuti mapudwe ake akhale ovuta.