Malawi News

Nkhondo idakalipo mu EPL

Nkhondo idakalipo mu EPL

Timu ya Manchester United yasokelera m’nkhalango ya Nottingham pomwe pa nthawi yomwe imakatulukira kuti njira ndi iyi, wawo wakale Anthony Elanga anali atawapanga kale chipongwe mkati mwa nkhalangoyi kuti asawone njira mu mphindi zisanu zoyambilira zomwe zapeleka mpata kwa Nottingham Forest kuti ikakamile pa nambala yachitatu ndi ma points ake 57.


Masewelo omwe anachitikira pa bwalo la City mu mzinda wa Nottingham, achititsa kuti kuyamba kwa masewelo a mu English Premier League (EPL) ma timu atapumulira, timu ya Manchester United itsakamile pa nambala 13 ndi ma points ake 37.


Nayo Arsenal yabweza chigwembe cha ma points chomwe chinalipo kufika pa 9 kuti apeze mithutha ya Liverpool yomwe ili patsogolo mu mndandanda ndi ma points ake 70.


Arsenal yafika pa ma points 61 kutsatira chipongwe chomwe yachitila anyamata a Fulham powagudubula 2-1 pa bwalo la Emirates, zigoli kuchoka kwa Bukayo Saka ndi Mikel Merino pomwe Fulham inapeza chotonthozera kuchokera kwa Rodrigo Muniz.


Saka wagoletsa chigoli m’masewelo ake oyamba atakhala pa mphasa ya kuvulala kwa miyezi yoposa itatu.


Chigoli cha Strand Larsen chapeleka mweya kwa Wolves pomwe yasasula Westhampton 1-0.


⚽ Nottingham 1-0 Manchester United
⚽ Arsenal 2-1 Fulham
⚽ Wolves 1-0 West Ham