
Zadziwika kuti woyimba Patience Namadingo yemwe pakatipa watchuka ndi nkhani yoti amatchaja K10 million kukaimba malo amodzi, Lachinayi sanatenge nawo K200,000 yomwe nyumba ya chifumu idapeleka kwa achinyamata omwe anakacheza ndi m’tsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera munzinda wa Blantyre.
Paja khoswe wapatsindwi adaulura wapadzala! Izi waulura ndi Refilwe Ntopa, m’modzi mwa omwe anali nawo pa mkumanowu yemwe walemba pa tsamba lake la X (twitter) kuti Chakwera atangotuluka m’chipinda momwe mudachitikira mwambowu, onse adawuzidwa kuti adikire kaye pang’ono, asanyamuke.
“Anatiuza kuti akufuna alongosole za mayendedwe athu. Ndiye timadikira kuti mayina athu ayitanidwe koma anthu ena monga Doc Namadingo, sanadikilire nawo koma ambiri tinadikira ndithu,” watero Ntopa wotopayo.
M’tsogoleriyu anayitana achinyamata 100 ku mkumanowu zomwe zikusonyeza kuti ndalama zokwana K20 million za misonkho ya aMalawi zinaperekedwa kwa achinyamatawa. Koma kuchotsapo K200,000 yomwe Namadingo sanapochere, ndekuti K19.8 million ndi yomwe nyumba ya chifumu yapeleka kwa achinyamatawa kupatula zofunikira zina.
Pamkumanowu, Namadingo anathambitsa ndi mafuso Chakwera omwe ambiri mwa iwo sanayankhidwe mwa mvemvemve. “Kodi ndinu wolonjezedwayo kapena tidikire wina?” Ilo lidali limodzi mwa mafunso omwe adakulitsa mutu Chakwera.
0 Comments