
Mzika ina ya dziko lino, a Stevens Prince Thengo yati ikufuna nthambi yowona zolowa komanso kutuluka m’dziko muno (Department of Immigration and Citizenship Services) imupatse ndalama yokwana K300 miliyoni ngati chipukuta misonzi.
Malingana ndi chikalata chochokera kwa ma loya a Thengo, pa 24 December 2024, mkuluyi adapita ku tchuthi m’dziko la Israel. Komabe, iye adagwidwa atangofika pa bwalo la ndege la Ben Gurion m’dzikolo, pomuganizira kuti adagwiritsa ntchito chiphaso chachinyengo.
Ngakhale izi zidali chonchi, a Thengo adali ndi chiphaso chomwe adapatsidwa ku nthambi yoona zolowa komanso kutuluka m’dziko lino ndipo adatsatira ndondomeko yonse yopezera chiphasochi.
Chikalatachi chatinso, atamangidwa m’dziko la Israel, iwo anabwezedwa m’dziko la Zambia koma anamangidwanso pa mlandu omwewo pa 25 December atangofika pa bwalo la ndege. Iwo akuti adatulutsidwa mchitokosi cha apolisi pa 28 December, 2024 maloya awo atalowelelapo pa nkhaniyi.
Pakadali pano, maloya oyimira a Thengo apereka miyezi itatu kuti nthambiyi ikhale itapereka chipukuta misonzichi ndipo kupanda kutero, iwo adzasumira boma.
Mzika zambiri za dziko lino zakhala zikudandaula kuti ziphaso zawo zoyendera zikumakanidwa m’maiko ena ponena kuti ndi zachinyengo.
0 Comments