Malawi News

Masikono atsike mtengo – Chithyola

Masikono atsike mtengo – Chithyola

Nduna ya Zachuma, a Simplex Chithyola Banda ati boma lachotsa msonkho wa 16.5% Value Added Tax (VAT) pa buledi (bread) ndi ma sikono (buns) ndipo akuyembekezera kuti mitengo ya Bread ndi mabanzi zitsika.


Izi zadziwika pamene ndunayi imapeleka ndondomeko ya zachuma yokwana 8.05 trillion Kwacha ya mchaka cha 2025/2026, kuchoka pa 6 trillion Kwacha ya mchaka cha 2024/2025 ku Nyumba ya Malamulo mu nzinda wa Lilongwe.


Mwa zina zomwe zili mu ndondomekoyi, Ndunayi inati ndalama yomwe amalandira ma intern omwe amagwira mu nthambi za boma ayikweza kuchoka pa 80,000 Kwacha kufika pa 150,000 Kwacha.


Iwo anatinso ndalama zokwana 60 billion Kwacha zipita ku ndondomeko yogulira chimanga mu ndondomeko ya zachuma ya 2025/2026 ndipo ati ayika ndalama zina kuti ADMARC itukuke m’magwiridwe ake a ntchito.


A Chithyola Banda anati pofika mwezi wa September, 2024, dziko la Malawi lidali lili ndi ngongole zokwana K16.19 trillion, zomwe zaimitsa mutu aMalawi ambiri.