Malawi News

Manchester United yaswa Leicester City

Manchester United yaswa Leicester City

Manchester United ya Ruben Amorim yayamba kuyenda kukwera mtunda tsopano pomwe pano ili pa nambala 13 ndi ma points ake 37 pomwe yaswa Leicester City 3-0 pa bwalo King Power, mu chikho cha English Premier league (EPL) lamulungu ku England.


Leicester yomwe yafa masewelo ake 13 mwa 14 omalizawa omwe yasewela, ikuphopholika kachikena ku chiwonongeko chotuluka league ya EPL, pamene zigoli za Rasmus Hojilund, Garnacho ndi Bruno Fernandes ndi zomwe zaliza Ruud Van Nistelrooy kumkankhiranso ku Championship.


English Premier league (EPL)

Nayo Arsenal ikulilira m’mimba kuti idachita chibwana ndi kuchitaya pa dzana, ngakhale yawaza Chelsea 1-0 pa bwalo la Emirates kudzera mu chigoli cha Mikel Merino pa mphindi ya chi 20 zinakhala zokwana kusiya kukamwa kwa wa Chelsea kakasi.


Arsenal tsopano yafika pa ma point 58 m’masewelo 29 kufanana ndi Liverpool yomwe ili ndi ma point 70, pamene Chelsea yakakamila pa nambala 4 ndi ma points ake 49 ndipo Chelsea yati ngakhale mpikisano pa ma point uli othithikana mu EPL, iwo khumbo ndi masomphenya awo ndi kufuna kusewela mu champions league season ikubwerayi.


Masewelo onse 1,2, 3 kwa 0, zonse zatha motele;


⚽ Arsenal 1- 0 Chelsea
⚽ Fulham 2-0 Tottenham
⚽ Leicester 0-3 Manchester United