
Phungu wa ku Nyumba ya Malamulo dera la Chiradzulu West Mathews Ngwale, wadandaula kuti aphungu akayima kupempha zitukuko ku ma unduna, unduna ukakhala opanda mayankho umawabwezera nkhani ya chitukukocho kuti aphungu apite nayo ku khonsolo pomwe ati makhonsolo amakhala opanda ndalama komanso akuthandizidwa ndi chuma chosakwana.
Phunguyu anayima kufunsa funso lowonjezera (supplementaly) pomwe anapempha kuti unduna umange youth resource centre pa Mbulumbudzi m’boma la Chiradzulu ndipo anayamba ndi kunena kuti ulendo uno chonde asamuuze kuti apitenso ku khonsolo ponena kuti khonsolo yake ilibe ndalama.

A Ngwale analankhula izi dzulo mnyumba ya malamulo mu nzinda wa Lilongwe, pomwe anafunsa funso pamwamba pa funso la phungu wa Chiradzulu central a MacTimes Malowa omwe anafunsa unduna wa zamasewelo ndi achinyamata kuti uganizire zomanga ‘Youth Resource Centre’ kwa mfumu yayikulu Likoswe m’boma la Chiradzulu ponena kuti ithandiza achinyamata ndi maluso osiyanasiyana.
Nduna ya za maboma ang’ono, a Richard Chimwendo Banda anayidumphira nkhaniyi ndi kunena kuti ma khonsolo akulandira ndalama zokwanira potchula ndalama monga za mthumba la Governance to Enable Service Delivery (GESD1), ndipo ati posachedwapa boma lalandiranso 70 million za ku America zopita ku ma khonsolo.
A Banda atinso posachedwapa ndalama zina za GESD-2, zikhale zikupitanso ku ma khonsolo.
Poyankha funso la phunguyu, nduna yowona za achinyamata ndi masewelo, a Uchizi Mkandawire ati nkhani yomanga ma ‘Youth Resource Centre’ adaitula ku ma khonsolo kotelo aphungu adzipita ndi nkhaniyi ku ma khonsolo, ponena kuti akatha kukagwiritsa nawo ntchito ndalama za mthumba la CDF, DDF mwa zina.
0 Comments