Malawi News

Katundu akupitilira kukwera pa msika

Katundu akupitilira kukwera pa msika

A Malawi akungoyenera kuvala zilimbe pomwe katundu osiyanasiyana akupitilira kukwera mtengo tsiku ndi tsiku. Katundu wambiri yemwe aMalawi amagwiritsa ntchito akunka nakwera ndipo anthu ambiri m’dziko muno akukhalira kudandaula.


Katundu monga mafuta ophikira pano akwera kwambiri. Mwachitsanzo mafuta ophikira a 5 litres a kukoma pano ndi 36,000 kwacha pomwe miyezi yapitayo anali pa K22,000.


Mafuta a 5 litres a Sunfoil pano ndi K44,000, pomwe 2 litres ya Sunfoil ndi K17, 000. Sitoko yemweyu opaka pa buledi wa blue band (1kg) pano ndi K15,500. Paketi ya sugar pano ndi 3000, ndipo ndiwo zomwe anthu ambiri amapulumukira soya pieces pano ndi 600 ma shop ena 800.


Ngakhale a Malawi ambiri akudandaula koma zikuwoneka kuti boma lomwe lilipori lilibe mayankho pa zakukwera kwa katundu ofunikirayu. Ndipo aMalawi akungoyenera kuzolowera kuti akapita ku gulosare azipeza mitengo yasitha tsiku lirilonse.


Chipani cha MCP chomwe chikulamura pano chati mitengo ya zinthu ikukwera kuti ena apeze pochitira ndale.


Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) yemwenso ndi sipikala wa Nyumba ya Malamulo a Catherine Gotani Hara, limodzi ndi nduna za zamigodi a Ken Zikhale Ng’oma ati anthu ena akukweza dala mitengo ya katundu mdziko muno ndi cholinga chofuna kupeza pochitira ndale ndi kuipitsa boma la kongelesi ndi Chakwera.