Malawi News

Ine za gospel zanuzo ayi – wasambwadza Peter Sambo

Woyimba Peter Sambo sanafune kubisa za ku khosi koma kulavula chichewa ponena kuti iye siwoyimba nyimbo zauzimu ndipo wasambwadza kuti oyimba nyimbo zauzimu ambiri ndi mimbulu koma amadzionetsa ngati nkhosa. “Ndilekeni ine ndili phee! Sindikupanga nawo za gospel zanuzo ndinasankha njira ina.”


Sambo yemwe amadziwika kwambiri ndi nyimbo za “Tachilowa Chaka China” komaso “Monga Mufunira,” wati sakufuna kumadzibisa ngati wauzimu kwambiri pomwe zisali choncho. Iye wati sakusamala kuti anthu adziti walowelera, koma bola ali pamtendere komaso ubale wake ndi “Jah Jah” uli bwino.


“Inetu ndinagwa, ndimamwa mowa komanso pena ndikasangalala embassy ndimagwira,” watelo Sambo. “Ndiye kuli ena ake kakaka kukakamira zoti ndine gospel artist, ndinasiya zosangalatsa anthu osayamika ine.”


Woyimbayu wati pano izitchedwa META4 ndipo akuzitchula kuti ndiwoyimba wamba osatiso woyimba nyimbo zauzimu monga momwe anthu amamudziwira.


META4 wadzudzulaso mchitidwe wa anthu oyimba nyimbo zauzimu womadziwonetsa ngati nkhosa koma akuchita kusaweluzika. “Munandikana mutamva ndimamwa mowa tsopano. Ma show anu munasiya kundiitana pomwe kuli zidakwa lololo ku gospel music Malawi kuti nditchule mayina pano anthu asiya kukumverani.”


Sambo waonjezeraso kuti, “azimayi a gospel mumawatama aja enanso ndi zidakwa zotheratu koma akaima ndikuvinitsa mbina kwinaku akulira inu nkumati pali uzimu pamenepa osadziwa akulira machimo apanga kuti apezeke pa stage ndi promoter.”