Anthu omwe anali a Payoniya mu ulamuliro wa chipani chimodzi cha Malawi Congress omwe mtsogoleri wake anali malemu Hastings Kamuzu Banda awopseza kuti achita m’bindikiro ku ma ofesi a boma Capital Hill ngati boma siliwalipira ndalama zawo kumapeto kwa mwezi uno.
Gululi lidatenga nawo mbali m’ndondomeko ya utumiki wa achinyamata m’dziko muno pomwe adachita nawo ntchito zodzipereka pa chitukuko cha dziko.
Izi zidapitilira mpaka asilikari a nkhondo a Malawi adalanda zida za achinyamatawa panthawi yomwe dziko lino lidasankha ulamuliro wa demokalase m’chaka cha 1993.
Patadutsa zaka makumi atatu (30) tsopano pomwe mamembala 800 omwe kale anali a gululi sanalandirebe ndalama zawo kuchokera ku boma, ngakhale ena adalandira kale.
Yemwe akuimira gulu la a Payoniyawa a Phillip Mwangonde adadandaula kuti ngakhale Nyumba yamalamulo idavomereza ndalama zambiri zolipilira achinyamatawa (omwe pano ndi achikulire), ambiri mwa iwo sadalandirebe phindu lawo.
Padakali pano akuluakulu a boma anakana kuyankha mafunso pankhaniyi ponena kuti nduna ya zachuma ipereka ndemanga pa bajeti yapakati pa chaka lachitatu ku Nyumba ya Malamulo ku Lilongwe.
Posachedwapa, komiti ya nyumba ya malamulo yoona za umoyo wa anthu, yaulula kuti boma lili ndi ngongole yokwana 60 biliyoni kwacha yomwe ikuyenera kubwezera anthu ogwira ntchito m’boma maka opuma pantchito.
0 Comments