Katswiri womwetsa zigoli mu timu ya dziko lino Flames, Gabadinho Mhango, watengera timu yake ya Marumo Gallants ku khothi pomwe akufuna ndalama zoposa K82 miliyoni kwacha kamba kogwiritsa ntchito zithuzi zake.
Malingana ndi tsamba la Soccer Betting News la m’dziko la South Africa, Mhango akuloza chala timu ya Marumo Gallants kuti yakhala ikugwiritsa ntchito zithuzi zake komaso dzina lake kangapo konse m’masamba anchezo koma osamupatsa ndalama za chipukuta misonzi.
Izi zikuphatikiza chithuzi chomwe timuyi idaika pa tsamba lake pa 5 December, 2023, pochemelera masewera ake ndi timu ya Orlando Pirates, kanema yemwe ankaonetsa Gaba akuyankhula yemwe adaikidwa pa 13 September, 2024, komaso kuikidwa kwa dzina lake pa mndandanda wa osewera oyambilira pa masewero ena ndipo mndandandawu udaikidwa pa masamba anchezo a timuyi pa 14 March, 2025.
Poyamba, wosewerayu adakatula madandaulo ake ku National Dispute Resolution Committee ya Premier Soccer League, yomwe idakana kumva nkhaniyi mwezi wa February kamba kosowa mphamvu za ulamuliro zomwe zidapangitsa kuti Mhango akamanga’ale ku bwalo la milandu.
M’mapepala a khothi, wosewera wakale wa Orlando Pirates-yu wati ali ndi ufulu wopindula pakugwiritsidwa ntchito kwa chithunzi chake, ma signature, dzina lake, mawu, komaso dzina lake loselewura.
Poyamba ufuluwu udali m’manja mwa kampani yomwe inkamuilira ya Prosport motsogozedwa ndi Michael Makaab ndipo atagulitsidwa ku timu ya Swallows FC pamtengo wa ndalama zokwana 828,000, Prosport idapereka ufulu kwa Mhango mu August 2023.
Mhango akuti timu ya Gallants, pomwe idagula Swallows, idatenga udindo wonse pa ufulu wake, koma wati timuyi yakhala ikulephera kulemekeza zomulipira. Mu January komaso September, 2024 Mhango adakumbutsa timuyi zoti akuyenera kulipidwa ZAR828,000 yomwe ndi pafupifupi K83 miliyoni koma timuyi siidamulipilebe ndalamazi mpaka lero.
0 Comments