Malawi News

EPL yayaka moto

EPL yayaka moto

Loto la timu ya Arsenal likusanduka loto la chumba pomwe chomwe ikufuna mu English Premier League (EPL) chikuoneka chawatelera kuposa mlamba. Izi zili delo kutsatira mpata wa ma points 13 omwe ulipo tsopano kuti agwirane ndi Liverpool kutsatira masewelo omwe Arsenal yagwirana pakhosi 0-0 ndi Nottingham Forest pa bwalo la City usiku wathawu.


Manchester United ndi osewera ake 10 yapambana pa Ipswich 3-2 koma movutika kwambiri kutsatira red card yomwe Patrick Dorgu analandira mchigawo choyamba pa mphindi ya chi 43, ndipo Harry Maguire ndi yemwe otsatira a timuyi akuyenera kumgwira chanza popatitsa chigoli chachitatu Man-U pa Old Trafford.


Liverpool yalengeza pa Arsenal kuti “Tatsogola ife mudzitipeza” pomwe yawamba Newcastle United 2-0, Szoboszlai ndi Mac Allista ndi omwe anapeleka mkuwe pa Anfield. Pomwe Erling Haaland ndi yekha yemwe anatangwanika kulinganiza Tottenham ya pa nambala 13 kuti ife 1-0 pakwawo.


Liverpool ili pa nambala 1 ndi ma points 67, Arsenal pa 2 ndi ma points 54, Nottingham 48, Manchester City 47, pomwe Manchester United yasintha kubwera pa nambala 14 ndi ma points 33 chetee.


Masewelo onse usiku wathawu:


⚽ Nottingham 0-0 Arsenal
⚽ Manchester United 3-2 Ipswich
⚽ Liverpool 2-0 Newcastle
⚽ Tottenham 0-1 Manchester City
⚽ Brentford 1-1 Everton