
Kutsatira mtsutso omwe wabuka pa zitukuko zomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera walengeza posachedwapa kuti boma lake lakwanilitsa, boma lalengeza kuti nduna zikhala zikutambasula bwino za zitukukozi.
Malingana ndi kalata yomwe boma latulutsa yosayinidwa ndi Colleen Zamba, mlembi wamkulu mu ofesi yamtsogoleri ndi nduna, ndunazi zikhala zikutambasula zitukukozi m’nyumba ya malamulo komanso m’njira zina.
Mu kalatayi, boma lati ndilodzipeleka kukwanilitsa malonjezo ake komanso kuonetsetsa kuti anthu akuuzidwa chilungamo pa nkhani ya zitukuko zosiyanasiyana m’dziko muno.
Kuyambira Lachisanu, anthu akhala akutsutsa zitukuko zomwe Chakwera analengeza kuti boma lake lakwanilitsa. Mwachitsanzo, anthu ku Likoma atsutsa kuti kumeneko kwamangidwa nyumba 28 za apolisi.
0 Comments