Malawi News

Anthu ena akufuna ine ndi a Chakwera tiyambane – Usi

Anthu ena akufuna ine ndi a Chakwera tiyambane – Usi

A Michael Usi omwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ati pali anthu ena amene akuyesetsa kuti iwo ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ayambane ndipo ati khalidwe lotelo limazunzitsa aMalawi, pamene ati kalikonse komwe iwo ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko amachita, a Chakwera amadziwa ndipo iwo ali ngati kapitawo m’munda mwa mtsogoleri wa dziko powathandiza.


M’mawu awo ku nyumba ya boma ya Mudi mu nzinda wa Blantyre dzulo, a Usi anati ena amene anali m’boma kale ndi omwe pano ayamba kuchuluka nzeru koma pa nthawi yawo sanapange kanthu.


A Usi anatinso nthawi yokopa anthu ikafika adzakhala akufotokozera anthu magwelo a mavuto ena monga kusowa kwa ndalama za kunja ndipo apempha anthu kuti asawasiye.


Iwo anaziguguda pa chifuwa kuti tsopano mafuta a galimoto ayamba kupezeka chifukwa iwo agwira gawo la public service delivery, ndipo ati aMalawi adekhe pa nkhani ya kukwera mitengo kwa katundu ponena kuti pali kagulu kena ka anthu komwe kakufuna kazizunza aMalawi posunga ndalama zakunja.


Iwo ati pakufunika kuti adindo ena achotsedwe ntchito ndipo ena amangidwe pa nkhani ya kukwera mitengo kwa katundu komwe aMalawi sakupuma nako tsiku lililonse.


Pa nkhani ya ndale a Usi ati ena akuti nsalu ya odya zake ndi ya UTM ndipo iwo ati nsaluyi si ya UTM.